Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.
Mateyu 16:22 - Buku Lopatulika Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Petro adamtengera pambali nayamba kumdzudzula. Adati, “Pepani Ambuye, zisatero ai. Mulungu asalole zimenezi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.” |
Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.
Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.