Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
Mateyu 16:17 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Ndiwe wodala, Simoni mwana wa Yona, pakuti si munthu wakuululira zimenezi ai, koma ndi Atate anga amene ali Kumwamba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anati kwa iye, “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba. |
Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.
Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.
kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi:
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;
chimene sanachizindikiritse ana a anthu m'mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu,
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;
Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:
Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.