Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.
Mateyu 16:15 - Buku Lopatulika Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anafunsa kuti, “Nanga inuyo mumati ndine yani?” |
Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.
Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Khristu.
Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu.