Mateyu 15:26 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.” |
Koma iye anati, Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;
kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.
Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.