Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Mateyu 15:25 - Buku Lopatulika Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!” |
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;
Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.
Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.
Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.
Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.
Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.