Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Mateyu 15:22 - Buku Lopatulika Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mai wina wachikanani, wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.” |
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.
Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
si kwa mitundu yambiri ya anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, amene sungathe kudziwitsa chinenedwe chao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.
Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.
Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.