Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
Mateyu 15:21 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adachoka kumeneko, napita ku madera a ku Tiro ndi Sidoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni. |
Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.
nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.
Asere sanaingitse nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Alabu, kapena a Akizibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobu;