Mateyu 15:17 - Buku Lopatulika Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi inu simuzindikira kuti zonse zoloŵa m'kamwa mwa munthu zimaloŵa m'mimba mwake, pambuyo pake nkukatayidwa kuthengo? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi? |
chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.
Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;
Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.