Mateyu 15:15 - Buku Lopatulika Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Petro adampempha kuti, “Timasulirenitu fanizoli.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Petro anati, “Timasulireni fanizoli.” |
Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.
Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo.
Ophunzira ake ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena chiphiphiritso.