Mateyu 15:13 - Buku Lopatulika Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Chomera chilichonse chimene sichidabzalidwe ndi Atate anga akumwamba, chidzazulidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe. |
Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho?
Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.
Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.
Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;