Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?
Mateyu 14:8 - Buku Lopatulika Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mai wake atamuuza choti apemphe, mwana wamkazi uja adati, “Mundipatse pompano mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” |
Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?
pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.
Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.
Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.
Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;
anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake.
Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe;
Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi.
Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale.