Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 14:7 - Buku Lopatulika

Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chilichonse akapempha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chilichonse akapempha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero Herode adaalonjeza molumbira kuti, “Ndithudi, ndidzakupatsa chilichonse chimene ungapemphe.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe.

Onani mutuwo



Mateyu 14:7
6 Mawu Ofanana  

Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.


Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.


Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.


Wotsinzina ndiye aganizira zokhota; wosunama afikitsa zoipa.


Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.


Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.