Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake.
Mateyu 14:6 - Buku Lopatulika Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi adaavina pamaso pa anthu oitanidwa ku phwando, mwakuti adaakondwetsa Herode kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri. |
Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake.
Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akulu ake onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.
Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.
nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.
Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.
Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha Inu.
Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.
Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa.
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;
Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita,
ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;