ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;
Mateyu 14:5 - Buku Lopatulika Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kwenikweni Herode ankafuna kupha Yohane, koma ankaopa anthu, chifukwa iwo ankati ndi mneneri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri. |
ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.
Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.
Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.
Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.