Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;
Mateyu 14:4 - Buku Lopatulika Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti Yohane adaauza Herode kuti, “Nkulakwira Malamulo kumukwatira mkaziyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.” |
Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;
Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.
Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Munthu akatenga mkazi wa mbale wake, chodetsa ichi; wavula mbale wake; adzakhala osaona ana.
Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.