Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.
Mateyu 14:23 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri yekha kukapemphera. M'mene kunkayamba kuda, nkuti ali komweko yekhayekha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. |
Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?
Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.