Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 14:21 - Buku Lopatulika

Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma tsono anthu amene adaadyawo analipo ngati zikwi zisanu amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.

Onani mutuwo



Mateyu 14:21
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.


Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.


Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.


Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.


Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa,


Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.


Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.