Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.
Mateyu 14:2 - Buku Lopatulika nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adauza nduna zake kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.” |
Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.
Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
Ndipo Herode chiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;
Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona.