Mateyu 14:18 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Bwera nazoni kuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.” |
Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.
Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.