Mateyu 14:16 - Buku Lopatulika Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu adaŵauza kuti, “Palibe chifukwa choti achokere. Inuyo apatseni chakudya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.” |
Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano.
Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.
Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.
Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.