Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake.
Mateyu 14:12 - Buku Lopatulika Ndipo ophunzira ake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ophunzira ake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake ophunzira a Yohane adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda. Kenaka adapita kukauza Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu. |
Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake.
Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi.