Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa mu Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.
Mateyu 14:11 - Buku Lopatulika Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutuwo adautengera m'mbale nakaupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake. |
Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa mu Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.
chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadane nao mwazi, mwazi udzakulondola.
Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.