koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.
Mateyu 14:10 - Buku Lopatulika ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adatuma munthu kuti akamdule mutu Yohaneyo m'ndende. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende. |
koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.
Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.
Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake.
Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe;
koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.
Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamchitiranso zilizonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.
Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona Iye.
Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa, ndi kupha izo.