Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.
Mateyu 13:56 - Buku Lopatulika Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi suja alongo ake onse ali nafe pompano? Nanga tsono zonsezi adazitenga kuti?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?” |
Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.