Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Mateyu 13:48 - Buku Lopatulika limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Likadzaza, anthu amalikokera ku mtunda. Tsono amakhala pansi, nsomba zabwino nkumaziika m'madengu, zachabe nkumangozitaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. |
Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;
Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.
Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.