Mateyu 13:45 - Buku Lopatulika Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati munthu wamalonda wonka nafunafuna ngale zokongola zamtengowapatali. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. |
Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;
ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.