Mateyu 13:35 - Buku Lopatulika kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, “Ndidzalankhula nawo m'mafanizo. Ndidzaulula zimene zinali zobisika chilengedwere dziko lapansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero zinakwaniritsidwa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri kuti, “Ndidzatsekula pakamwa panga ndi mafanizo, ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwa dziko lapansi.” |
Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.
Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.
Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse.
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,
chimene sanachizindikiritse ana a anthu m'mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu,
ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;
Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.