Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa.
Mateyu 13:34 - Buku Lopatulika Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zonsezi Yesu adalankhula ndi anthu aja m'mafanizo. Sadalankhule nawo kanthu popanda fanizo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankhula zinthu zonsezi kwa gulu la anthu mʼmafanizo ndipo Iye sananene kalikonse kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. |
Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa.
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.
Ophunzira ake ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena chiphiphiritso.