koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.
Mateyu 13:27 - Buku Lopatulika Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’ |
koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.
Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi?
Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;
Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,
koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.