Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera mu Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?
Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.