Mateyu 13:19 - Buku Lopatulika Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu aliyense akamva mau onena za Ufumu wakumwamba, koma osaŵamvetsa, Woipa uja amabwera nkudzalanda zimene zidafesedwa mumtima mwake. Zimenezi ndiye mbeu zogwera m'njira zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira. |
Momwemo ufanana ndi yani mu ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni m'munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?
Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;
Ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.
Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo.
ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako,
Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye.
Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.
koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.
Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.
Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;
kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.
Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.
osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.
Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.