Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;
Mateyu 13:14 - Buku Lopatulika Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi iwoŵa zikuchitikadi zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “ ‘Kumva mudzamva ndithu, koma osamvetsa, kuyang'ana mudzayang'ana ndithu, koma osapenya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa: “ ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa. Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu. |
Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;
Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.
kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.
Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.
Koma sanamvere Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?
koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.
koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.