Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.
Mateyu 13:13 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthuŵa ndimalankhula nawo m'mafanizo, chifukwa ngakhale amapenya, komabe saona, ndipo ngakhale amamva, komabe samva kwenikweni kapena kumvetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo: “Ngakhale akupenya koma saona, ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira. |
Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.
Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;
Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.
monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.