Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani, ndipo abale anga ndi ayani?
Mateyu 12:49 - Buku Lopatulika Ndipo anatambalitsa dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatambalitsa dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero, adaloza ophunzira ake nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo akuloza ophunzira ake, Iye anati, “Awa ndiwo amayi anga ndi abale anga. |
Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani, ndipo abale anga ndi ayani?
Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.
Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.