Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Mateyu 12:23 - Buku Lopatulika Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onse adazizwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi ameneyu sangakhale Mwana uja wa Davide?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu onse anadabwa ndipo anati, “Kodi uyu ndi kukhala mwana wa Davide?” |
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:
Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.
Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele.
Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?