Mateyu 12:19 - Buku Lopatulika Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye sadzachita makani, kapena kufuula. Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sadzalimbana, sadzafuwula, ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake mʼmakwalala. |
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.
Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;