Mateyu 12:16 - Buku Lopatulika nawalimbitsira mau kuti asamuwulule Iye; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nawalimbitsira mau kuti asamuwulule Iye; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma adaŵalamula kuti asakamuulule. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero nawachenjeza kuti asamuwulule kuti yani. |
Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.
Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.
Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense.
Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,
Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.