Mateyu 12:14 - Buku Lopatulika Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo kuti apangane njira yophera Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere. |
Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;
Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:
Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.
Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.
Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.
Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye.