akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Mateyu 12:13 - Buku Lopatulika Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero, adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino ngati linzake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale. |
akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.
Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.