Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
Mateyu 12:10 - Buku Lopatulika ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'menemo munali munthu wopuwala dzanja. Tsono anthu ena amene ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, adamufunsa kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mʼmenemo munali munthu wolumala dzanja. Pofuna chifukwa chokamunenezera, iwo anamufunsa Yesu kuti, “Kodi nʼkololedwa kuchiritsa munthu tsiku la Sabata?” |
Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.
Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata.
Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?
Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.
nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeze pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;
Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.
Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.
Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?
Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.