Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.
Mateyu 11:24 - Buku Lopatulika Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga iwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu.” |
Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.
Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga, ikula koposa tchimo la Sodomu, umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng'ono wako sanachite, iye kapena ana ake aakazi, monga umo unachitira iwe ndi ana ako aakazi.
Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.
Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu.
Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.