Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo.
Mateyu 11:20 - Buku Lopatulika Pomwepo Iye anayamba kutonza mizindayo, m'mene zinachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa kuti siinatembenuke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa kuti siinatembenuke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Yesu adayamba kudzudzula midzi imene Iye adaaichitira zamphamvu zochuluka. Adaidzudzula chifukwa anthu ake anali osatembenuka mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yesu anayamba kudzudzula mizinda imene zodabwitsa zake zambiri zinachitikamo, chifukwa chakuti sinatembenuke mtima. |
Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo.
Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.
Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.
kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
nachitira mwano Mulungu wa mu Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalape ntchito zao.
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.
Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake.