Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Mateyu 11:16 - Buku Lopatulika Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Kodi mʼbado uwu ndingawufanizire ndi chiyani? Uli ngati ana opezeka mʼmisika amene akuyitana anzawo nʼkumati: |
Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.
Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.
Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.
Ndipo m'chiphunzitso chake ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika,
Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?
Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika.
Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani?