Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.
Mateyu 11:14 - Buku Lopatulika Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ngati mukufunadi kukhulupirira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngati inu mufuna kulandira izi, iyeyu ndi Eliya amene ankanena kuti adzabwera uja. |
Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.
Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.