Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Mateyu 11:13 - Buku Lopatulika Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aneneri onse ndiponso Malamulo a Mose ankaneneratu za Ufumu umenewu mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti aneneri onse ndi malamulo ananenera kufikira nthawi ya Yohane. |
Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.
Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.
Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni;