Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
Mateyu 11:10 - Buku Lopatulika Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyu ndi amene malemba akunena za iye kuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu amene adzakonza njira yanu. |
Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.
Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.
Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.
Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.