Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.
Mateyu 10:42 - Buku Lopatulika Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.” |
Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.
Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikaponyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo.
Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.
Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.