Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga.
Mateyu 10:39 - Buku Lopatulika Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza. |
Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga.
Pakuti aliyense amene akafuna kupulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma aliyense amene akataya moyo wake chifukwa cha Ine, iye adzaupulumutsa uwu.
Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha.
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.