Mateyu 10:31 - Buku Lopatulika Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri. |
Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!