Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
Mateyu 10:30 - Buku Lopatulika komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. |
Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.
komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.
Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.
Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi mu Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pamutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe.